Unduna wa maboma ang’onoang’ono wati makhonsolo ndi okonzeka kuyendetsa thumba la ndalama za chitukuko la CDF pogwiritsa ntchito ndondomeko zomwe zakhazikitsidwa. Boma lidatulutsa ndondomekozo kumayambiliro kwa sabata ino kufufuta nkhawa zoti CDF ikhoza kukumana ndi zokhoma chifukwa nduna ya za chuma a Joseph Mwanamvekha adalephera kupereka ndondomekozo m’Nyumba ya Malamulo. Mneneri wa undunawo a
Unduna wa maboma ang’onoang’ono wati makhonsolo ndi okonzeka kuyendetsa thumba la ndalama za chitukuko la CDF pogwiritsa ntchito ndondomeko zomwe zakhazikitsidwa. Boma lidatulutsa ndondomekozo kumayambiliro kwa sabata ino kufufuta nkhawa zoti CDF ikhoza kukumana ndi zokhoma chifukwa nduna ya za chuma a Joseph Mwanamvekha adalephera kupereka ndondomekozo m’Nyumba ya Malamulo. Mneneri wa undunawo a Chimwemwe Njoloma ati ndondomekozo zidafika kale m’makhonsolo ndipo akuluakulu a m’makhonsolowo adaphunzitsidwa kale za momwe ndondomekozo zingagwirire ntchito.
“Palibe chotsamwitsa chilichonse, makhonsolo ndi okonzeka kuyendetsa CDF pogwiritsa ntchito ndondomeko zatsopano. Ndondomekozo alinazo kale tikunena pano,” atero a Njoloma. Malingana ndi ndondomekozo, makomiti a kumidzi motsogozedwa ndi akuluakulu a pa khonsolo, ndiwo azipanga ziganizo za zitukuko ku dera kwawo pomwe makhansala ndi aphungu ntchito yawo ikhala kalondolondo.
Ndondomekozo zikuunikiranso n t c h i t o zomwe CDF ingagwiritsidwe ntchito monga momwe khonsolo ingagulire galimoto ndi njinga zogwiritsa ntchito pa khonsolo. “Boma lomwe lili ndi madera a a p h u n g u osaposa ikhoza kugula galimoto imodzi pomwe makhonsolo omwe ali ndi aphungu oposa asanu akhoza kugula galimoto ziwiri komanso dera la phungu aliyense likhoza kukhala ndi njinga yamoto imodzi,” zikutero ndondomekozo. Koma mkulu wa bungwe loyang’anira makhonsolo la Malawi Local Government Assoc i a t ion ( M a l g a ) a H a d r o d Mkandawire atsutsa zoti makhonsolo ndi okonzeka kuyendetsa CDF pogwiritsa ntchito ndondomekozo.
Iwo ati makhonsolowo sadalandilebe ndondomeko zomwe zikunenedwazo komanso ngakhale atalandira, mpofunika maphunziro oyenera kuti azitha kuyendetsa thumbalo. “Ndondomekozo zisadafike m’ma k h o n s o l o koma n s o sangangotumiza ndondomeko popanda maphunziro chifukwa ndalamazi ndi zambiri, ena mwa omwe ali m’makomiti oyendetsa thumbalo sadayang’anireko ndalama zochuluka choncho,” atero a Mkandawire. Kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu m’chilungamo a Willy Kambwandira ati makhonsolo komanso makomiti oyendetsa CDF ndi ofunika maphunziro akayendetsedwe ka ndalama za boma kuti CDF ikhaledi ya phindu.
“Kuyendetsa ndalama za boma kumasiyana ndi kuyendetsa ndalama za munthu. Pali masitepe omwe ndalama za boma zimadutsa kuti zikafike kwa anthu ndiye zonsezo nzoyenera makomitiwo ataphunzira,” adatero a Kambwandira. Ndondmekozo zikuunikira kuti ndalama za CDF zizichokera ku akaunti ya boma kupita ku banki yaikulu ya Reserve yomwe izitumiza ndalamazo ku maakaunti a makhonsolo malingana ndi zitukuko zomwe akonza.
Ndondomekozo zidakonzedwa ndi unduna wa za chuma komanso unduna wa za chi lungamo mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika atakana kusaina lamulo loti aphungu ndiwo aziyendetsa thumbalo. Mwamphamvu zina zomwe ndondomekozo zapereka kwa anthu a kumudzi ndi kukapereka ma l ipoti pomwe aona kut i ndalamazo sizikugwiritsidwa ntchito motsata ndondomeko kapena ngati kontirakita akuonetsa ukambelembele. A Mutharika atalengeza zoti ndalama za CDF zakwera kuchoka pa K200 miliyoni kufika pa K5 biliyoni, mafumu akuluakulu adayamikira kuti ndalama za chitukuko zapitadi kumudzi.
“Apapa zakhala bwino ndipo mphamvu ku anthu zija n’zimenezi. Chofunika tsopano ndi maphunziro a omwe aziyendetsa ndalamazo kuti zitukuko zizioneka,” adatero a Inkosi M’mbelwa a ku Mzimba.
