Bwalo la milandu ku Zomba lakana kupereka belo kwa Senior Chief Malemia komanso kuyeza DNA kuti adziwe mimba imene mfumuyo idathandizira mtsikanayo kuchotsa idali ya ndani. Woweruza a Elijah Daniels adauza bwalolo kuti lakana kupereka belo chifukwa zichedwetsa kumaliza mlanduwo. Akuyankha mlandu: A Malemia Kuchokera pa 25 March pamene mfumuyo, imene dzina lawo la pa msonkho ndi Clement Lloyd idamangidwa, kameneka ndi kachitatu kukanidwa belo.
Malinga ndi chigamulo chimene bwalolo lidapereka pa 7 April chaka chino, mfumuyo idapezeka ndi milandu iwiri: Wogonana ndi mtsikana wachichepere komanso kuthandizira kuchotsa mimba. Ndipo a Daniels adakana pempho la woimira mfumuyo a Patrick Debwe kuti pasayezedwe DNA chifukwa milandu akuyankhayo palibepo wofufuza kuti mimbayo ndi ya ndani. “Ndondomeko zoyeza DNA zikhonza kuchedwetsa mlandu,” adatero iwo. Bwalolo lapereka mwayi kwa woimirira mfumuyo kuti akhonza kukachita apilo zimene bwalolo lagamula ndipo mlanduwo udzalowanso pa 5 May 2026 pamene a Debwe adzayambe kuteteza mfumuyo.
